Mabungwe omenyera ufulu pa nkhani za ubeleki apempha adindo kukambilanabe za bill yolola amayi kutchotsa pakati

Amayi ndi asungwana ambiri akupitilira kutaya mimba pogwiritsa ntchito njira zosayenera ngakhale m’chitidwewu uli oletsedwa malinga ndi malamulo a dziko lino zomwe zikuika pachiopsezo miyoyo yawo.

Mkulu wa bungwe la Peace to Community Liberty and Development, Faida Imran-Phiri ndiyemwe wayankhula izi pamkumano wa achinyamata, mafumu komanso adindo ochokera m’madela a mfumu yaikulu Kulunda m’boma la Salima.

Phiri wati ndizomvetsa chisoni kuti imfa zochuluka zokhudza ubeleki zikuchitika pakati pa amayi komanso atsikana omwe akumagwiritsa ntchito njira zosayenera pochotsa mimba zomwe gwero lake likumakhala mavuto kupangitsa boma kuwononga ndalama zochuluka kugulira zipangizo m’zipatala zothandizira amayi omwe achotsa mimbawa koma anakumana ndi mavuto monga kutsalidwa, kutaya magazi ndi zina, zomwe zikanathandizira pantchito zina zofunika.

“nzodandaulitsa kuti ngakhale lamulo limakaniza amayi kuchotsa mimba anthu akuchitabe mchitidwewu mobisa, gwero lake ndilakuti mavuto akawapeza pamene zakanika amabwera kuchipatala kuti adzathandizidwe. Boma likutaya ndalama zomwe likanatha kugwiritsa ntchito pazitukuko zina patakhala lamulo loloreza amayi kuchotsa mimba movomelezeka popeza iwo akhoza kumathandizidwa moyenera,” iye anatero.

Phiri anapitiliza kunena kuti mkumanowu cholinga chake unali kusonkhanitsa onse okhudzidwa ndi nkhani zaubereki kuti akambirane momwe angabwerere pamodzi ndikukweza mfuwu kupempha a phungu ku nyumba yamalamulo kuti athe kukambirana za bill yoloreza amayi kuchotsa pakati ngati pali zifukwa zina zokwanira ndikukhazikitsa biluyi kukhala lamulo.

“Tikufunanso timve zikhulupiliro zomwe zinakhazikika m’midzimu pankhani zochotsa mimba ndimomwe anthu omwe azindikiridwa kuti achotsa pakati amatengeredwera. Tikuzindikira kuti kubwera pamodzi kwa magulu onse okhudzidwa ndikugundana mitu kukhoza kuthandizira kuti mfuwu wathu umveke patali pokakamiza aphungu kuti bilu imeneyi ikambidwe ndikuti tithe kupulumutsa miyoyo yomwe ikutaikayi,” anatero Phiri.

M’mawu ake, m’modzi mwa atsikana omwe anachotsapo pakati koma anasankha kuti asatchulidwe dzina anati iye akupitiliza kukumanabe ndi mavuto ena pamoyo wake ngakhale papita zaka chichotsereni mimbayi.

“ndinachotsa pakati pomwa mankhwala m’chaka cha 2023 kamba koti mamunayo anandikana koma mkadafa poti nnataya magazi ochuluka. Ndinachita mwayi poti anathamangira nane kuchipatala nsanga komwe anakandikolopa koma mpaka pano ndimapangabe chizungulire,” iye anatero.

Mgwirizano wamabungwe oyang’anira za ubereki ndi maufulu a achinyamata wa Alliance for Youth in SRHR Organisations (AYSO) ukulimbikitsa adindo kutenga gawo ndikumema aphungu kuonjezera zifukwa zina zolora amayi kuchotsa pakati m’dziko muno. Malingana ndi kafukufuku yemwe bungwe la Centre for Solutions Journalism (CSJ) linachita linaonetsa kuti chiwerengero cha anthu omwe amachotsa mimba pogwiritsa ntchito njira zosayenera ndichokwera mmaiko omwe lamulo silimalora kuchotsa pakati ngati dziko la Malawi kusiyana ndi m’maiko omwe lamulo limalora.

KuMalawi kuno amayi oposa 80 pa 100 aliwonse apabanja ndiomwe amachotsa pakati. Mwaiwo, amayi pafupifupi 65 pa 100 aliwonse ngakumudzi omwe amagwiritsa ntchito njira zosayenera. Amayi 28 pa 100 aliwonse akuti ndiomwe amapeza thandizo lokhudza ubereki nzipatala za boma kamba koti achotsa mimba.

(Wolemba: Jean Chilombo)

Related posts

WHO Urges Malawi to Strengthen Fight Against Zoonotic Diseases

First Lady Urges Greater Digital Inclusion for Girls and Women

Salima District Council Honours Outgoing MPS And Councilors