Mfumu Nkhumpha yochokera kwa T/A Maganga m’boma la Salima yalangiza anthu omwe akhale akupikisana pa chisankho chachipulula chofuna kupeza yemwe adzayimile chipani cha Malawi Congress (MCP) m’chigawo chapakati cha bomali kuwonetsetsa kuti asunga bata ndi mtendele.
Iwo ayankhula izi lachitatu pamene m’modzi mwa omwe akufuna kupikisana nawo, a James Manyetera amawonekela kwa atsogoleri a chipani cha MCP m’dela la Nsangu ndi Kaphatenga.
Malinga ndi a Mkumpha, atsogoleri akuyenera kulimbikitsa bata ndi mtendere pamene dziko lino likukonzekera chisankho.
Poyankhula pa nkumanowu, a James Manyetera ati awonetsetsa kuti otsatira awo akusunga bata komanso mtendere, ndipo kupititsa patsogolo nkhani ya demokalase.
“Chisakho chimabwera komanso kupita koma dela lapakati m’boma la Salima linabwera kudzakhazikika, ndipo chisankho chi chikupereka mwayi kwa otsatira chipani chi kuwonetsa kukhwima nzeru pa nkhani ya demokalase,” a Manyetera adafotokoza.
A Manyetera, adawonjezera ponena kuti anthu akuyenera kukhulupilira nfundo zawo zomwe ndi kuchepetsa ulova, kupititsa patsogolo ntchito za ulimi, umoyo, maphunziro komanso ufulu wa amayi ndi ana mwa zina.
“Nditagwira ntchito boma kwa nthawi yayitala,ndawona kuti tsopano nthawi yakwana yoti, ndikatumikire anthu akwanthu. Ndizosabisa kuti dela lapakati boma la Salima ntchito za chitukuko sizikupita patsogolo, “atero a Manyetera.
A Manyetera apemphanso anthu m’dziko muno kudzavotera mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera pa chisankho chomwe chilipo chaka chino, ponena kuti a Chakwera awonetsa kudzipereka kwawo pa ntchito yopititsa patsogolo umoyo ndi chisamaliro cha a Malawi.
Chipani cha MCP chidayamba ntchito yochotitsa zisankho zachipulula mmwezi wa February chaka chino ndicholinga chofuna kupeza anthu omwe adzayimile chipanichi ngati aphungu komanso makhansala.
(Wolemba: Alinafe Nyanda)